-
Yeremiya 39:5-7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Koma asilikali a Akasidi anawathamangitsa ndipo Zedekiya anamupeza mʼchipululu cha Yeriko.+ Anamugwira nʼkupita naye kwa Mfumu Nebukadinezara* ya Babulo ku Ribila,+ mʼdziko la Hamati,+ kumene Nebukadinezara anamuweruza. 6 Zitatero mfumu ya Babulo inapha ana aamuna a Zedekiya ku Ribila, Zedekiyayo akuona. Inaphanso anthu onse olemekezeka a ku Yuda.+ 7 Mfumu ya Babulo inachititsa khungu maso a Zedekiya ndipo kenako inamumanga mʼmaunyolo akopa* kuti apite naye ku Babulo.+
-
-
Danieli 5:18, 19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Inu mfumu, Mulungu Wamʼmwambamwamba anapatsa bambo anu Nebukadinezara ufumu, ukulu, ulemu ndi ulemerero.+ 19 Chifukwa chakuti Mulungu anamupatsa ukulu umenewu, anthu a mitundu yonse komanso anthu olankhula zinenero zosiyanasiyana ankanjenjemera chifukwa cha mantha pamaso pake.+ Aliyense amene ankafuna kumupha ankamupha, amene ankafuna kumusiya ndi moyo ankamusiya ndipo aliyense amene ankafuna kumukweza ankamukweza, amene ankafuna kumutsitsa ankamutsitsa.+
-