5 Ansembewo akadzaliza malipenga a nyanga za nkhosa pa ulendo wa 7, ndipo inu mukadzamva kulira kwa malipengawo, nonse mudzafuule mwamphamvu mfuu yankhondo, ndipo mpanda wonse wa mzindawo udzagwa mpaka pansi.+ Pamenepo, nonsenu mudzathamangire kumeneko.”