10 Komanso Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedayo,+ amene ankapha nsomba limodzi ndi Simoni anadabwa kwambiri. Koma Yesu anauza Simoni kuti: “Usachite mantha. Kuyambira lero uzisodza anthu amoyo.”+ 11 Choncho ngalawazo anafika nazo kumtunda, ndipo iwo anasiya chilichonse nʼkumutsatira.+