13 Kenako Paulo ndi anzakewo, anayamba ulendo wa panyanja kuchoka ku Pafo, ndipo anakafika ku Pega, ku Pamfuliya. Koma Yohane+ anawasiya nʼkubwerera ku Yerusalemu.+ 14 Atachoka ku Pega anakafika ku Antiokeya wa ku Pisidiya. Kumeneko analowa mʼsunagoge+ tsiku la Sabata nʼkukhala pansi.