-
Maliko 7:20-22Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Iye ananenanso kuti: “Chotuluka mʼthupi la munthu nʼchimene chimaipitsa munthu.+ 21 Chifukwa mumtima mwa anthu+ mumatuluka maganizo oipa ngati: zachiwerewere,* zakuba, zopha anthu, 22 zachigololo, dyera, kuchita zoipa, chinyengo, khalidwe lopanda manyazi,* diso la kaduka, mawu onyoza, kudzikweza ndiponso kuchita zinthu mopanda nzeru.
-