-
Mateyu 17:10-13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Koma ophunzirawo anamufunsa kuti: “Nanga nʼchifukwa chiyani alembi amanena kuti Eliya ayenera kubwera choyamba?”+ 11 Iye anayankha kuti: “Inde, Eliya adzabweradi ndipo adzabwezeretsa zinthu zonse.+ 12 Komabe, ine ndikukuuzani kuti Eliya anabwera kale koma iwo sanamuzindikire ndipo anamuchitira zilizonse zimene iwo anafuna.+ Iwo adzazunzanso Mwana wa munthu mwa njira imeneyi.”+ 13 Atatero ophunzirawo anazindikira kuti akunena za Yohane Mʼbatizi.
-