-
Luka 11:29-32Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
29 Pamene gulu la anthulo linkachulukirachulukira, iye anayamba kunena kuti: “Mʼbadwo uwu ndi mʼbadwo woipa, ukufuna chizindikiro. Koma sudzapatsidwa chizindikiro chilichonse kupatulapo chizindikiro cha Yona chokha.+ 30 Mofanana ndi Yona+ amene anakhala chizindikiro kwa anthu a ku Nineve, Mwana wa munthu adzakhalanso chizindikiro ku mʼbadwo uwu. 31 Mfumukazi yakumʼmwera+ adzaiukitsa kwa akufa pa Tsiku la Chiweruzo limodzi ndi anthu a mʼbadwo uwu ndipo idzawatsutsa, chifukwa mfumukazi imeneyi inabwera kuchokera kumalekezero a dziko lapansi kudzamva nzeru za Solomo. Koma tsopano wina woposa Solomo ali pano.+ 32 Anthu a ku Nineve adzauka pa Tsiku la Chiweruzo limodzi ndi mʼbadwo uwu ndipo adzautsutsa, chifukwa iwo analapa atamva ulaliki wa Yona.+ Koma tsopano wina woposa Yona ali pano.
-