Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Maliko 4:3-9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 “Tamverani! Wofesa mbewu anapita kukafesa mbewu.+ 4 Pamene ankafesa, mbewu zina zinagwera mʼmbali mwa msewu ndipo kunabwera mbalame nʼkuzidya. 5 Zina zinagwera pamiyala pamene panalibe dothi lokwanira ndipo zinamera mwamsanga chifukwa dothilo linali losazama.+ 6 Koma dzuwa litawala kwambiri zinawauka ndipo zinafota chifukwa zinalibe mizu. 7 Mbewu zina zinagwera paminga ndipo mingazo zinakula nʼkulepheretsa mbewuzo kukula moti sizinabereke chipatso chilichonse.+ 8 Koma zina zinagwera panthaka yabwino ndipo zinamera nʼkukula, moti zinayamba kubereka zipatso. Mbewu ina inabereka zipatso 30, ina 60 ndipo ina 100.”+ 9 Kenako anawonjezera mawu akuti: “Amene ali ndi makutu akumva, amve.”+

  • Luka 8:4-8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Ndiyeno gulu lalikulu la anthu litasonkhana, limodzi ndi ena amene ankamulondola kuchokera mʼmizinda yosiyanasiyana, Yesu anafotokoza fanizo lakuti:+ 5 “Wofesa mbewu anapita kukafesa mbewu zake. Pamene ankafesa, zina zinagwera mʼmbali mwa msewu nʼkupondedwapondedwa ndipo zinadyedwa ndi mbalame zamumlengalenga.+ 6 Zina zinagwera pathanthwe. Koma zitamera, zinauma chifukwa panalibe chinyezi.+ 7 Mbewu zina zinagwera paminga ndipo mingazo zinkakulira limodzi ndi mbewuzo ndipo zinalepheretsa mbewuzo kukula.+ 8 Koma zina zinagwera panthaka yabwino, ndipo zitakula, zinabereka zipatso kuwirikiza maulendo 100.”+ Atanena zimenezi, analankhula mokweza mawu kuti: “Amene ali ndi makutu akumva, amve.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena