20 Koma imene inafesedwa pamiyala, ndi munthu amene wamva mawu nʼkuwavomereza mwamsanga ndiponso mosangalala.+ 21 Komabe chifukwa chakuti amakhala alibe mizu amapitiriza kukula kwa nthawi yochepa. Koma akakumana ndi masautso kapena kuyamba kuzunzidwa chifukwa cha mawuwo, iye amapunthwa mwamsanga.