-
Maliko 7:25-30Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Nthawi yomweyo, mayi wina amene mwana wake wamkazi anagwidwa ndi mzimu wonyansa anamva za iye ndipo anabwera nʼkudzagwada pamapazi ake.+ 26 Mayiyu anali Mgiriki, wa Chisurofoinike. Iye anapempha Yesu mobwerezabwereza kuti atulutse chiwanda mwa mwana wakeyo. 27 Koma Yesu anauza mayiyo kuti: “Choyamba, zimafunika kuti ana akhute kaye, chifukwa si bwino kutenga chakudya cha ana nʼkuponyera tiagalu.”+ 28 Koma mayiyo anamuyankha kuti: “Inde mbuyanga, komatu tiagalu timadya nyenyeswa za anawo pansi pa tebulo.” 29 Yesu atamva zimenezo anauza mayiyo kuti: “Chifukwa chakuti wanena zimenezi, pita, chiwandacho chatuluka mwa mwana wakoyo.”+ 30 Choncho anapita kunyumba kwake ndipo anakapeza mwanayo atagona pabedi chiwandacho chitatuluka.+
-