33 “Tsopano tikupita ku Yerusalemu ndipo Mwana wa munthu akaperekedwa kwa ansembe aakulu ndi alembi. Iwo akamuweruza kuti aphedwe ndipo akamupereka kwa anthu amitundu ina. 34 Iwo akamuchitira chipongwe, kumulavulira, kumukwapula ndi kumupha, koma pakadzapita masiku atatu, adzauka.”+