-
Maliko 11:4-6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Choncho iwo ananyamuka ndipo anapezadi bulu wamphongo atamumangirira pakhomo, mʼmphepete mwa msewu waungʼono. Ndipo iwo anamasula buluyo.+ 5 Koma ena mwa anthu amene anali ataimirira chapomwepo anawafunsa kuti: “Cholinga chanu nʼchiyani pomasula buluyu?” 6 Iwo anawauza zimene Yesu ananena ndipo anawalola kuti apite.
-
-
Luka 19:32-35Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
32 Choncho anthu amene anatumidwawo ananyamuka ndipo anakamupezadi mmene iye anawauzira.+ 33 Koma pamene ankamasula buluyo, eniake anawafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukumasula buluyu?” 34 Iwo anayankha kuti: “Ambuye akumufuna.” 35 Pamenepo iwo anamutenga nʼkupita naye kwa Yesu. Kenako iwo anaponya malaya awo akunja pabuluyo ndipo Yesu anakwerapo.+
-