-
Maliko 11:15, 16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Tsopano iwo anafika ku Yerusalemu. Kumeneko analowa mʼkachisi nʼkuyamba kuthamangitsa anthu amene ankagulitsa ndi kugula zinthu mʼkachisimo, ndipo anagubuduza matebulo a anthu amene ankasintha ndalama komanso mabenchi a anthu amene ankagulitsa nkhunda.+ 16 Iye sanalole aliyense kuti adutse mʼkachisimo atanyamula katundu.
-