-
Maliko 11:27-33Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
27 Kenako anafikanso ku Yerusalemu. Ndipo pamene ankayenda mʼkachisi, ansembe aakulu, alembi ndi akulu anabwera 28 nʼkumufunsa kuti: “Kodi muli ndi ulamuliro wochitira zinthu zimenezi? Kapena ndi ndani amene anakupatsani ulamuliro umenewu?”+ 29 Yesu anawayankha kuti: “Ndikufunsani funso limodzi. Mundiyankhe, ndipo inenso ndikuuzani amene anandipatsa ulamuliro umene ndimachitira zimenezi. 30 Kodi ubatizo umene Yohane ankachita+ unali wochokera kumwamba kapena kwa anthu? Ndiyankheni.”+ 31 Choncho iwo anayamba kukambirana kuti: “Tikanena kuti, ‘Unachokera kumwamba,’ atifunsa kuti, ‘Nanga nʼchifukwa chiyani simunamukhulupirire?’ 32 Koma tinganene kuti ‘Unachokera kwa anthuʼ ngati?” Iwo ankaopa gulu la anthu, chifukwa anthu onsewo ankakhulupirira kuti Yohane analidi mneneri.+ 33 Choncho iwo anayankha Yesu kuti: “Sitikudziwa.” Yesu anawauza kuti: “Inenso sindikuuzani amene anandipatsa ulamuliro umene ndimachitira zimenezi.”
-
-
Luka 20:1-8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Tsiku lina akuphunzitsa anthu mʼkachisi komanso kulengeza uthenga wabwino, kunabwera ansembe aakulu, alembi limodzi ndi akulu 2 nʼkudzamufunsa kuti: “Tiuzeni, kodi muli ndi ulamuliro wochitira zinthu zimenezi? Kapena ndi ndani amene anakupatsani ulamuliro umenewu?”+ 3 Yesu anawayankha kuti: “Inenso ndikufunsani funso limodzi ndipo mundiyankhe: 4 Kodi ubatizo umene Yohane ankachita unachokera kumwamba kapena kwa anthu?” 5 Choncho iwo anayamba kukambirana kuti: “Tikanena kuti, ‘Unachokera kumwamba,’ iye atifunsa kuti, ‘Nanga nʼchifukwa chiyani simunamukhulupirire?’ 6 Koma tikanena kuti, ‘Unachokera kwa anthu,’ anthu onsewa atiponya miyala, chifukwa iwo amakhulupirira ndi mtima wonse kuti Yohane anali mneneri.”+ 7 Choncho anayankha kuti sakudziwa kumene unachokera. 8 Yesu anawauza kuti: “Inenso sindikuuzani amene anandipatsa ulamuliro umene ndimachitira zimenezi.”
-