18 Koma onse anayamba kupereka zifukwa zokanira.+ Woyamba anamuuza kuti, ‘Ine ndagula munda ndipo ndikuyenera kupita kukauona. Pepani sinditha kubwera.’ 19 Wina ananena kuti, ‘Ine ndagula ngʼombe 10 zapagoli ndipo ndikupita kukaziyesa. Pepani sinditha kubwera.’+