35 Koma amene aonedwa kuti ndi oyenerera kudzapeza moyo pa nthawi imeneyo nʼkudzaukitsidwa kwa akufa sadzakwatira kapena kukwatiwa.+ 36 Komanso iwo sadzafanso, chifukwa adzakhala ngati angelo. Iwo adzakhalanso ana a Mulungu pokhala ana a kuuka kwa akufa.