-
Luka 4:9-12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Kenako anapita naye ku Yerusalemu ndipo anamukweza pamwamba pa khoma la mpanda wa kachisi* nʼkumuuza kuti: “Ngati ndinu mwana wa Mulungu, mudziponye pansi kuchokera pano.+ 10 Paja Malemba amati, ‘Iye adzalamula angelo ake zokhudza inu, kuti akutetezeni,’ 11 ndipo ‘Adzakunyamulani mʼmanja mwawo, kuti phazi lanu lisawombe mwala.’”+ 12 Poyankha Yesu anamuuza kuti: “Malemba amati, ‘Yehova* Mulungu wanu musamamuyese.’”+
-