Maliko 14:36 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 36 Kenako anati: “Abba,* Atate,+ zinthu zonse nʼzotheka kwa inu. Ndichotsereni kapu iyi. Komatu osati mwa kufuna kwanga, koma mwa kufuna kwanu.”+ Luka 22:42 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 42 kuti: “Atate, ngati mukufuna, ndichotsereni kapu iyi. Komatu zimene mukufuna zichitike, osati zofuna zanga.”+ Yohane 5:30 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 30 Ine sindingachite chilichonse chimene ndangoganiza pandekha. Ndimaweruza mogwirizana ndi zimene ndamva, ndipo chiweruzo changa nʼcholungama,+ chifukwa sindichita zofuna zanga, koma zofuna za amene anandituma.+ Yohane 6:38 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 38 Chifukwa ndinabwera kuchokera kumwamba+ kudzachita zofuna za amene anandituma, osati zofuna zanga.+ Aheberi 10:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Ananenanso kuti: “Taonani! Ine ndabwera kudzachita chifuniro chanu.”+ Akuchotsa dongosolo loyambalo kuti akhazikitse lachiwiri.
36 Kenako anati: “Abba,* Atate,+ zinthu zonse nʼzotheka kwa inu. Ndichotsereni kapu iyi. Komatu osati mwa kufuna kwanga, koma mwa kufuna kwanu.”+
42 kuti: “Atate, ngati mukufuna, ndichotsereni kapu iyi. Komatu zimene mukufuna zichitike, osati zofuna zanga.”+
30 Ine sindingachite chilichonse chimene ndangoganiza pandekha. Ndimaweruza mogwirizana ndi zimene ndamva, ndipo chiweruzo changa nʼcholungama,+ chifukwa sindichita zofuna zanga, koma zofuna za amene anandituma.+
38 Chifukwa ndinabwera kuchokera kumwamba+ kudzachita zofuna za amene anandituma, osati zofuna zanga.+
9 Ananenanso kuti: “Taonani! Ine ndabwera kudzachita chifuniro chanu.”+ Akuchotsa dongosolo loyambalo kuti akhazikitse lachiwiri.