-
Maliko 14:55-59Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
55 Ndiyeno ansembe aakulu ndi Khoti lonse Lalikulu la Ayuda ankafunafuna umboni kuti anamizire Yesu mlandu nʼcholinga choti amuphe, koma sanaupeze.+ 56 Anthu ambiri ankapereka umboni wabodza kuti amunamizire mlandu,+ koma maumboni awowo ankatsutsana. 57 Komanso, anthu ena ankaimirira nʼkumapereka umboni womunamizira kuti: 58 “Ife tinamva iyeyu akunena kuti, ‘Ine ndidzagwetsa kachisi uyu amene anamangidwa ndi manja ndipo mʼmasiku atatu okha ndidzamanga wina osati womangidwa ndi manja.’”+ 59 Komabe ngakhale pa mfundo zimenezi, umboni wawo sunali wogwirizana.
-