-
Deuteronomo 21:22, 23Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
22 Ngati munthu wachita tchimo loyenera chiweruzo choti aphedwe,+ ndiyeno munthuyo waphedwa, ndipo mwamupachika pamtengo,+ 23 mtembo wake usamakhale pamtengopo usiku wonse.+ Mʼmalomwake, muzionetsetsa kuti mwamuika mʼmanda tsiku lomwelo, chifukwa munthu aliyense wopachikidwa pamtengo ndi wotembereredwa ndi Mulungu.+ Musamaipitse dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti likhale cholowa chanu.”+
-