40 Choncho iwo anatenga mtembo wa Yesu nʼkuukulunga ndi nsalu zamaliro zonunkhira,+ mogwirizana ndi mwambo umene Ayuda ankatsatira poika maliro. 41 Tsopano kumalo kumene anamupachikirako kunali munda mmene munali manda atsopano,+ ndipo anali asanaikemo munthu chiyambire.