-
Mateyu 14:6-12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Koma tsiku lokumbukira kubadwa kwa Herode+ litafika, mwana wamkazi wa Herodiya anavina pa tsikulo ndipo anasangalatsa kwambiri Herode,+ 7 moti anachita kulumbira polonjeza mtsikanayo kuti adzamupatsa chilichonse chimene angapemphe. 8 Ndiyeno mtsikanayo, mayi ake atachita kumuuza zoti apemphe ananena kuti: “Mundipatse mutu wa Yohane Mʼbatizi mʼmbale pompano.”+ 9 Mfumuyo inamva chisoni koma poganizira lumbiro limene inapanga lija komanso anthu amene anali nawo paphwandolo, analamula kuti mutuwo uperekedwe. 10 Choncho anatuma munthu kuti akadule mutu wa Yohane mʼndende. 11 Kenako anabweretsa mutuwo mʼmbale nʼkuupereka kwa mtsikanayo ndipo iye anapita nawo kwa mayi ake. 12 Pambuyo pake ophunzira ake anabwera kudzatenga mtembo wake nʼkukauika mʼmanda. Kenako anapita kukauza Yesu.
-