Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Mateyu 14:15-21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Koma chakumadzulo ophunzira ake anabwera kwa iye nʼkunena kuti: “Kuno nʼkopanda anthu ndipo nthawi yatha, auzeni anthuwa kuti anyamuke, apite mʼmidzimo kuti akagule chakudya choti adye.”+ 16 Koma Yesu anawayankha kuti: “Palibe chifukwa choti apitire. Inuyo muwapatse chakudya.” 17 Iwo anamuuza kuti: “Tilibe chilichonse pano, kupatulapo mitanda 5 ya mkate ndi nsomba ziwiri zokha basi.” 18 Iye anati: “Bweretsani zimenezo kuno.” 19 Kenako analamula gulu la anthulo kuti likhale pansi pa udzu. Ndiyeno anatenga mitanda ya mkate 5 ndi nsomba ziwiri zija nʼkuyangʼana kumwamba ndi kupemphera.+ Atatero ananyemanyema mitanda ya mkate ija nʼkuipereka kwa ophunzirawo ndipo iwo anagawira gulu la anthulo. 20 Choncho onse anadya nʼkukhuta ndipo zimene zinatsala anazitolera moti zinadzaza madengu 12.+ 21 Koma amene anadya anali amuna pafupifupi 5,000 osawerengera akazi ndi ana aangʼono.+

  • Luka 9:12-17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Komano nthawi inali chakumadzulo. Choncho atumwi 12 aja anabwera kwa iye nʼkunena kuti: “Kuno nʼkopanda anthu ndipo nthawi yatha, auzeni anthuwa kuti anyamuke, apite mʼmidzi ndi mʼmadera ozungulira kuti akapeze malo ogona komanso chakudya choti adye.”+ 13 Koma iye anawayankha kuti: “Inuyo muwapatse chakudya.”+ Iwo anati: “Tilibe chilichonse kupatulapo mitanda ya mkate isanu ndi nsomba ziwiri zokha basi. Kapenatu tipite kukagula chakudya chokwanira anthu onsewa.” 14 Panali amuna pafupifupi 5,000 ndipo Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Uzani anthuwa kuti akhale mʼmagulu a anthu 50.” 15 Ophunzirawo anachitadi zimenezo, moti anthu onsewo anakhala pansi. 16 Kenako anatenga mitanda ya mkate 5 ndi nsomba ziwiri zija nʼkuyangʼana kumwamba ndipo anadalitsa chakudyacho. Atatero ananyemanyema mitanda ya mkateyo nʼkuipereka kwa ophunzira ake kuti aipereke kwa anthuwo. 17 Choncho onse anadya nʼkukhuta, ndipo anatolera zotsala zodzaza madengu 12.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena