Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Mateyu 16:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Kuyambira nthawi imeneyo, Yesu anayamba kuuza ophunzira ake kuti iyeyo akuyenera kupita ku Yerusalemu. Kumeneko akazunzidwa kwambiri ndi akulu, ansembe aakulu ndi alembi ndipo akaphedwa, koma pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa.+

  • Mateyu 17:22, 23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Atasonkhana pamodzi ku Galileya, Yesu anawauza kuti: “Mwana wa munthu adzaperekedwa mʼmanja mwa anthu+ 23 ndipo adzamupha. Koma pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa.”+ Atamva zimenezi iwo anamva chisoni kwambiri.

  • Maliko 8:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Komanso anayamba kuwaphunzitsa kuti Mwana wa munthu akuyenera kukumana ndi mavuto ambiri ndiponso kukanidwa ndi akulu, ansembe aakulu ndi alembi. Ndipo adzaphedwa+ nʼkuukitsidwa patapita masiku atatu.+

  • Luka 9:44, 45
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 44 “Mvetserani mosamala ndipo muzikumbukira mawu awa, chifukwa Mwana wa munthu adzaperekedwa mʼmanja mwa anthu.”+ 45 Koma ophunzirawo sanamvetse zimene anawauzazo. Tanthauzo lake linali lobisika kwa iwo kuti asazindikire ndipo ankaopa kumufunsa za mawu amenewa.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena