29 Yesu anawauza kuti: “Ndithu ndikukuuzani, palibe amene wasiya nyumba, mkazi, azichimwene, makolo kapena ana, chifukwa cha Ufumu wa Mulungu+ 30 amene sadzapeza zochuluka kwambiri kuposa zimenezi mu nthawi ino, ndipo mu nthawi imene ikubwerayo, adzapeza moyo wosatha.”+