-
Levitiko 14:10, 11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Pa tsiku la 8, iye adzatenge nkhosa zazingʼono zamphongo ziwiri zopanda chilema komanso nkhosa yaingʼono yaikazi+ imodzi yopanda chilema, yosapitirira chaka chimodzi. Adzatengenso ufa wosalala wokwana magawo atatu mwa magawo 10 a muyezo wa efa,* monga nsembe yake ya mbewu+ yothira mafuta ndi muyezo umodzi* wa mafuta.+ 11 Ndipo wansembe amene wagamula kuti munthuyo ndi woyera, azionetsa amene akudziyeretsayo, limodzi ndi zinthu zakezo kwa Yehova, pakhomo la chihema chokumanako.
-