-
Mateyu 22:42-45Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
42 “Mukuganiza bwanji za Khristu? Kodi ndi mwana wa ndani?” Iwo anayankha kuti: “Ndi mwana wa Davide.”+ 43 Iye anawafunsanso kuti: “Nanga nʼchifukwa chiyani mouziridwa ndi mzimu,+ Davide anamutchula kuti Ambuye, pamene ananena kuti, 44 ‘Yehova* anauza Ambuye wanga kuti: “Khala kudzanja langa lamanja mpaka nditaika adani ako pansi pa mapazi ako”’?+ 45 Ndiye ngati Davide anamutchula kuti Ambuye, zikutheka bwanji kuti akhale mwana wake?”+
-
-
Luka 20:41-44Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
41 Ndiyeno iye anawafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani amanena kuti Khristu ndi mwana wa Davide?+ 42 Chifukwa Davideyo ananena mʼbuku la Masalimo kuti, ‘Yehova* anauza Ambuye wanga kuti: “Khala kudzanja langa lamanja 43 mpaka nditaika adani ako kuti akhale chopondapo mapazi ako.”’+ 44 Choncho Davide anamutchula kuti Ambuye. Ndiye zikutheka bwanji kuti akhale mwana wake?”
-