Salimo 41:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Ngakhale munthu amene ndinkakhala naye mwamtendere, amene ndinkamukhulupirira,+Munthu amene ankadya chakudya changa, watukula chidendene chake nʼkundiukira.+ Mateyu 26:21, 22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Akudya chakudyacho iye ananena kuti: “Ndithu ndikukuuzani, mmodzi wa inu andipereka.”+ 22 Chifukwa chomva chisoni kwambiri ndi zimenezi, aliyense anayamba kumufunsa kuti: “Ambuye, kodi ndine kapena?” Luka 22:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Koma taonani! Wondipereka ndili naye limodzi patebulo pompano.+ Luka 22:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Choncho anayamba kukambirana pakati pawo za amene anakonza chiwembu chimenecho.+ Yohane 13:21, 22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Atanena zimenezi, Yesu anavutika kwambiri mumtima, ndipo anachitira umboni kuti: “Ndithu ndikukuuzani, mmodzi wa inu andipereka.”+ 22 Ophunzirawo anayamba kuyangʼanizana chifukwa sankadziwa kuti akunena ndani.+
9 Ngakhale munthu amene ndinkakhala naye mwamtendere, amene ndinkamukhulupirira,+Munthu amene ankadya chakudya changa, watukula chidendene chake nʼkundiukira.+
21 Akudya chakudyacho iye ananena kuti: “Ndithu ndikukuuzani, mmodzi wa inu andipereka.”+ 22 Chifukwa chomva chisoni kwambiri ndi zimenezi, aliyense anayamba kumufunsa kuti: “Ambuye, kodi ndine kapena?”
21 Atanena zimenezi, Yesu anavutika kwambiri mumtima, ndipo anachitira umboni kuti: “Ndithu ndikukuuzani, mmodzi wa inu andipereka.”+ 22 Ophunzirawo anayamba kuyangʼanizana chifukwa sankadziwa kuti akunena ndani.+