-
Ekisodo 26:31-33Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
31 Upange katani+ ya ulusi wabuluu, ya ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri. Pakataniyi upetepo akerubi. 32 Katani imeneyi uipachike pazipilala 4 za mtengo wa mthethe zokutidwa ndi golide. Tizitsulo tokolowekapo kataniyi tikhale tagolide. Zipilala zimenezi zikhale pazitsulo 4 zasiliva. 33 Kataniyi uipachike mʼmunsi mwa ngowe zolumikizira nsalu zapamwamba pa chihema, ndipo uike likasa la Umboni+ kuseri kwa kataniyi. Kataniyi ikhale malire a Malo Oyera+ ndi Malo Oyera Koposa.+
-