16 Pamene tinkakudziwitsani za mphamvu za Ambuye wathu Yesu Khristu komanso zokhudza kukhalapo* kwake, sitinatengere nkhani zabodza zimene anthu amapeka mochenjera. Koma tinakuuzani zinthu zokhudza ulemerero wake zimene tinachita kuona ndi maso athu.+