-
Mateyu 3:7-10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Yohane ataona Afarisi ndi Asaduki+ ambiri akubwera ku ubatizowo, anawauza kuti: “Ana a njoka inu,+ ndi ndani wakuchenjezani kuti muthawe mkwiyo umene ukubwerawo?+ 8 Ndiyetu mubale zipatso zosonyeza kulapa. 9 Musamadzinamize kuti, ‘Tili ndi atate wathu Abulahamu.’+ Chifukwa ndikukuuzani kuti Mulungu akhoza kupangira Abulahamu ana kuchokera kumiyala iyi. 10 Nkhwangwa yaikidwa kale pamizu yamitengo. Choncho mtengo uliwonse wosabereka zipatso zabwino udulidwa nʼkuponyedwa pamoto.+
-