5 Tamverani! Tsiku la Yehova lalikulu ndi lochititsa mantha lisanafike,+ ndidzakutumizirani mneneri Eliya.+ 6 Iye adzachititsa mitima ya abambo kubwerera kwa ana awo+ ndi mitima ya ana kubwerera kwa abambo awo. Adzachita zimenezi kuti ine ndisabwere kudzawononga dziko lapansi.”