14 Koma mtsogoleri wa sunagoge ataona zimenezi, anakwiya chifukwa Yesu anachiritsa munthu pa Sabata. Choncho anauza gulu la anthu kuti: “Pali masiku 6 amene tikuyenera kugwira ntchito.+ Muzibwera masiku amenewo kudzachiritsidwa, osati tsiku la Sabata.”+