-
Mateyu 8:8, 9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Mtsogoleri wa asilikali uja anayankha kuti: “Ambuye, sindine munthu woyenera kuti inu mukalowe mʼnyumba mwanga, koma mungonena mawu okha ndipo wantchito wangayo achira. 9 Chifukwa inenso ndili ndi akuluakulu ondiyangʼanira komanso ndili ndi asilikali amene ndimawayangʼanira. Ndikauza mmodzi kuti, ‘Pita!’ amapita, wina ndikamuuza kuti, ‘Bwera!’ amabwera. Kapolo wanga ndikamuuza kuti, ‘Chita ichi!’ amachita.”
-