-
Afilipi 2:9-11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Pa chifukwa chimenechi, Mulungu anamukweza nʼkumupatsa udindo wapamwamba+ ndipo mokoma mtima anamupatsa dzina loposa lina lililonse.+ 10 Anachita zimenezi kuti mʼdzina la Yesu, onse apinde mawondo awo, kaya ali kumwamba, padziko lapansi kapena pansi pa nthaka.*+ 11 Komanso kuti aliyense avomereze poyera kuti Yesu Khristu ndi Ambuye,+ zimene zidzapereka ulemerero kwa Mulungu Atate.
-