-
Mateyu 23:23, 24Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, anthu achinyengo inu! Chifukwa mumapereka chakhumi cha timbewu ta minti, dilili ndi chitowe,+ koma mumanyalanyaza zinthu zofunika za mʼChilamulo, zomwe ndi chilungamo,+ chifundo+ ndi kukhulupirika. Kupereka zinthu zimenezi nʼkofunika ndithu, koma osanyalanyaza zinthu zinazo.+ 24 Atsogoleri akhungu inu,+ amene mumasefa zakumwa zanu kuti muchotsemo kanyerere+ koma mumameza ngamila.+
-