-
Mateyu 23:29-31Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
29 Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, anthu achinyengo inu!+ Chifukwa mumamanga manda a aneneri ndi kukongoletsa manda* a anthu olungama,+ 30 ndipo mumanena kuti, ‘Tikanakhalako mʼmasiku a makolo athu, ifeyo sitikanakhudzidwa ndi mlandu wawo wokhetsa magazi a aneneri.’ 31 Choncho mukudzichitira nokha umboni kuti ndinu ana a anthu amene anapha aneneri.+
-