24 Komabe, moyo wanga sindikuuona ngati wofunika kwa ine. Chimene ndikungofuna nʼchakuti ndimalize kuthamanga mpikisanowu, komanso kuti ndimalize+ utumiki umene ndinalandira kwa Ambuye Yesu. Ndikungofuna kuchitira umboni mokwanira za uthenga wabwino wa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.