31 Choncho musamade nkhawa+ nʼkumanena kuti, ‘Tidya chiyani?’ kapena, ‘Timwa chiyani?’ kapenanso, ‘Tivala chiyani?’+ 32 Chifukwa anthu a mitundu ina akufunafuna mwakhama zinthu zonsezi. Koma Atate wanu wakumwamba akudziwa kuti inuyo mumafunikira zinthu zonsezi.