-
Mateyu 9:10, 11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Nthawi inayake, pamene ankadya chakudya* mʼnyumba ina, kunabwera anthu ambiri okhometsa msonkho komanso ochimwa ndipo anayamba kudya* limodzi ndi Yesu ndi ophunzira ake.+ 11 Koma Afarisi ataona zimenezi anafunsa ophunzira ake kuti: “Nʼchifukwa chiyani mphunzitsi wanu amadya limodzi ndi anthu okhometsa msonkho komanso ochimwa?”+
-
-
Maliko 2:15, 16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Nthawi inayake, ankadya chakudya* mʼnyumba mwa Levi ndipo anthu ambiri okhometsa msonkho komanso ochimwa ankadya limodzi ndi Yesu ndiponso ophunzira ake. Kumeneko kunali anthu ambiri amene ankamutsatira.+ 16 Koma alembi a Afarisi, ataona kuti Yesu akudya limodzi ndi anthu ochimwa ndi okhometsa msonkho, anayamba kufunsa ophunzira ake kuti: “Bwanji akudya limodzi ndi okhometsa msonkho komanso anthu ochimwa?”
-
-
Luka 5:29, 30Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
29 Kenako Levi anakonzera Yesu phwando lalikulu kunyumba kwake. Kumeneko kunabwera anthu ambiri okhometsa msonkho komanso ochimwa ndipo ankadya* limodzi ndi Yesu komanso ophunzira ake.+ 30 Afarisi ndi alembi awo ataona izi, anayamba kungʼungʼudza nʼkufunsa ophunzira ake kuti: “Nʼchifukwa chiyani inu mumadya ndi kumwa limodzi ndi okhometsa msonkho komanso anthu ochimwa?”+
-