12 Mukuganiza bwanji? Ngati munthu ali ndi nkhosa 100 ndipo imodzi mwa nkhosazo nʼkusochera,+ kodi sangasiye nkhosa 99 zija mʼphiri nʼkupita kukafunafuna yosocherayo?+ 13 Akaipeza, ndithu ndikukuuzani, amasangalala kwambiri ndi nkhosa imeneyo kusiyana ndi nkhosa 99 zimene sizinasochere zija.