6 Mpheta 5 amazigulitsa makobidi awiri ochepa mphamvu, si choncho? Komatu palibe ngakhale imodzi mwa mbalame zimenezi imene Mulungu amaiiwala.+ 7 Ndipotu ngakhale tsitsi lonse lamʼmutu mwanu amaliwerenga.+ Musachite mantha, ndinu ofunika kwambiri kuposa mpheta zambiri.+