-
Mateyu 20:25-27Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Koma Yesu anawaitana nʼkuwauza kuti: “Inu mukudziwa kuti olamulira a anthu a mitundu ina amapondereza anthu awo ndipo akuluakulu amasonyeza mphamvu zawo pa iwo.+ 26 Sizikuyenera kukhala choncho pakati panu.+ Koma aliyense amene akufuna kuti akhale wamkulu pakati panu akuyenera kukhala mtumiki wanu+ 27 ndipo amene akufuna kuti akhale woyamba pakati panu akuyenera kukhala kapolo wanu.+
-
-
Maliko 10:42-44Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
42 Koma Yesu anawaitana nʼkuwauza kuti: “Inu mukudziwa kuti amene amaoneka ngati* akulamulira anthu a mitundu ina, amapondereza anthu awo ndipo akuluakulu awo amasonyeza mphamvu zawo pa iwo.+ 43 Sizikuyenera kukhala choncho pakati panu. Koma aliyense amene akufuna kuti akhale wamkulu pakati panu akuyenera kukhala mtumiki wanu+ 44 ndipo amene akufuna kuti akhale woyamba pakati panu akuyenera kukhala kapolo wa onse.
-