-
Luka 9:46-48Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
46 Kenako iwo anayamba kukangana zokhudza amene anali wamkulu pakati pawo.+ 47 Yesu atazindikira zimene ankaganiza mumtima mwawo, anatenga mwana wamngʼono nʼkumuimika pambali pake. 48 Ndiyeno anawauza kuti: “Aliyense amene walandira mwana wamngʼono ngati uyu mʼdzina langa walandiranso ine. Ndipo aliyense amene walandira ine walandiranso amene anandituma.+ Chifukwa aliyense amene amachita zinthu ngati mwana wamngʼono pakati panu ndi amene ali wamkulu.”+
-