-
Levitiko 12:6, 7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Masiku a kuyeretsedwa kwake chifukwa chobereka mwana wamwamuna kapena wamkazi akakwana, azibweretsa kwa wansembe, pakhomo la chihema chokumanako, nkhosa yaingʼono yamphongo yosapitirira chaka chimodzi kuti ikhale nsembe yopsereza.+ Azibweretsanso mwana wa nkhunda kapena njiwa kuti ikhale nsembe yamachimo. 7 Wansembeyo aziipereka kwa Yehova ndi kumʼphimbira machimo ndipo mkaziyo adzakhala woyera pa kukha magazi kwake. Limeneli ndi lamulo lokhudza mkazi amene wabereka mwana wamwamuna kapena wamkazi.
-