-
Luka 9:7-9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Tsopano Herode,* wolamulira chigawo,* anamva zonse zimene zinkachitika. Iye anathedwa nzeru chifukwa ena ankanena kuti Yohane waukitsidwa.+ 8 Koma ena ankanena kuti Eliya waonekera. Enanso ankanena kuti mmodzi wa aneneri akale wauka.+ 9 Ndiyeno Herode anati: “Yohane ndinamudula mutu.+ Nanga amene akuchita zomwe ndikumvazi ndi ndani?” Choncho ankafunitsitsa atamuona.+
-