15 Koma iwo anafuula kuti: “Muthane naye! Muthane naye! Apachikidwe ameneyo!” Pilato anawafunsa kuti: “Kodi ndipachike mfumu yanu?” Ansembe aakulu anayankha kuti: “Tilibe mfumu ina koma Kaisara.” 16 Kenako anamupereka kwa iwo kuti akamuphe pomupachika pamtengo.+
Tsopano Yesu anali mʼmanja mwawo.