17 Iye ananyamula yekha mtengo wozunzikirapo nʼkutuluka kupita kumalo amene ankatchulidwa kuti Chibade,+ koma pa Chiheberi ankatchulidwa kuti Gologota.+ 18 Kumeneko anamupachika pamtengo+ limodzi ndi amuna ena awiri, wina mbali iyi, wina mbali inayi, Yesu pakati.+