-
Ekisodo 23:14, 15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Katatu pa chaka muzindichitira chikondwerero.+ 15 Muzichita Chikondwerero cha Mikate Yopanda Zofufumitsa.+ Muzidya mikate yopanda zofufumitsa masiku 7 pa nthawi imene inaikidwa mʼmwezi wa Abibu*+ mogwirizana ndi zimene ndinakulamulani, chifukwa munatuluka mu Iguputo mʼmwezi umenewu. Ndipo palibe amene ayenera kuonekera kwa ine chimanjamanja.+
-
-
Deuteronomo 16:16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Mwamuna aliyense pakati panu azikaonekera katatu pa chaka pamaso pa Yehova Mulungu wanu, pamalo amene Mulungu adzasankhe. Azikaonekera pa Chikondwerero cha Mkate Wopanda Zofufumitsa,+ Chikondwerero cha Masabata+ ndi pa Chikondwerero cha Misasa.+ Palibe aliyense wa iwo amene akuyenera kukaonekera kwa Yehova chimanjamanja.
-