19 Choncho poyankha Yesu anawauza kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, Mwana sangachite chilichonse chimene wangoganiza payekha, koma chokhacho chimene waona Atate wake akuchita.+ Chifukwa zilizonse zimene Atatewo amachita, Mwana amachitanso zomwezo mofanana ndi mmene Atatewo amachitira.